MABWALO A BULLETS NDI WANDERERS AYAMBA KUMANGIDWA
Matimu a FCB Nyasa Big Bullets ndi Mighty Mukuru Wanderers atha kuyamba kumwemwetera tsopano pomwe boma kudzera mwa nduna ya achinyamata ndi zamasewero, Uchizi Mkandawire, wati boma laika K800 million pa ntchitoyi.
Ndunayi yati pa ndondomeko ya ndalama zomwe zigwire ntchito mu zaka za 2023 kufikira 2024, boma layika ndalamazi ndi cholinga choti ntchitoyi iyambe kuyenda.
Mabwalowa anaperekedwa ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino, Professor Peter Mutharika, ndipo ntchito yomanga mabwalowa inaima kamba koti mtsogoleriyu anachotsedwa mu boma.
Boma linakonzanso bwalo Lina lomwe ankafuna kumanga nthawi ya utsogoleri wa Mutharika ndipo tsopano zinasiyidwa mu ulamulo wa boma la Malawi Congress Party.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores