NTOPWA IDZIWA OKUMANA NAWO MU MASEWERO OPITIRA KU CHAMPIONS LEAGUE LACHINAYI
Timu ya mpira wamiyendo koma ali amayi ya Ntopwa, ikuyembekezeka kudziwa matimu omwe akumane nawo mu masewero opitira ku chikho cha CAF Women's Champions League ku mbali ya kummwera kwa Africa lachinayi pomwe bungwe la COSAFA lichitse mayere a mpikisanowu patsikuli.
Bungwe la COSAFA lalengeza nkhaniyi lolemba pomwe tsopano kwatsala masiku ochepa kuti masewerowa achitike kuti apeze timu yomwe itapite ku Ivory Coast.
Matimu asanu ndi atatu (8) ndi omwe atenge nawo mbali mu mpikisanowu ndipo timu ya Ntopwa inafika ku ndimeyi kamba kokhala akatswiri achikho cha mdziko muno. Mayerewa achitikire mdziko la South Africa ndipo matimu ayikidwa mu magulu awiri.
Ntopwa ikhala timu yoyamba yaku Malawi kukasewera mu mpikisanowu pomwe akaonekere koyamba ndipo kuli matimu ena monga Mamelodi Sundowns, Green Buffaloes, Coastal do Sol, Double Action, Olympic de Moroni, Young Buffaloes ndi Lesotho Defense Force.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores