HARRY NYIRENDA WATSANZIKA KU HAMMERS
Mtsogoleri wa timu ya Ekwendeni Hammers, Harry Nyirenda, watsanzika kutimu yakeyi pomwe tsopano wachoka kutimuyi kukayang'ana mwayi ku matimu ena.
Imodzi mwa tsamba lolemba nkhani mdziko muno, Wa Ganyu, yatsimikiza za nkhaniyi ponena kuti Nyirenda watsanzika pomwe zamveka kuti apita ku timu Ina.
Iwo ati timu ya Civo United yatsegula zokambirana ndi katswiriyu ndipo amapatsa zomwe angakwanitse kumupatsa katswiriyu ndipo alingalira pomwe matimu enanso awiri akumufuna.
Nyirenda anapita ku timuyi mu chaka cha 2019 pomwe anachotsedwa ku timu ya Mighty Mukuru Wanderers yomwe anapitako mu 2016 atachoka ku Black Leopards yaku South Africa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores