MAPOINTSI ATATU KUTI CHITIPA IFIKE PAMWAMBA
Timu ya Chitipa United ikusiyana ma pointsi atatu okha ndi omwe akutsogolera ligi ya TNM, FCB Nyasa Big Bullets pomwe anachita kuchokera kumbuyo kuti agonjetse Mighty Wakawaka Tigers 2-1 pa bwalo la Karonga loweruka.
Stimella Muyira anamwetsa pa penate pa mphindi 74 kuti abwenze Chigoli cha Zikani Munthali cha mchigawo choyamba ndipo Rajab Nyirenda anamwetsa chigoli chopambanira pa mphindi 85 kuti asunge malo a pachitatu mwa mphamvu.
Mphunzitsi watimuyi, MacDonald Mtetemera anali okondwa atapambana masewerowa ponena kuti apambana mmasewero ovuta kwambiri.
"Chiyambireni ndine okondwa chifukwa tapambana masewero ovuta kwambiri, ndimadziwa kuti Tigers indizunguza poti imandidziwa kunja ndi mkati koma tithokoze Mulungu anatipatsa nzeru mchigawo chachiwiri kuti tipeze chipambano." Anatero Mtetemera.
Kutsatira kupambana kumeneko, Chitipa ili ndi mapointsi 23 pomwe yasewera masewero 13 ndipo ikutsalira ndi atatu okha kuti ipeze Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores