"BULLETS IMAYENERA KUGONJA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati ndi okondwa ndi mmene anyamata ake anasewerera mmasewero awo ndi Dedza Dynamos pomwe wati kufanana mphamvu ndi timuyi ndi mwayi poti amayenera kugonja.
Munthali amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi inachokera kumbuyo kawiri kuti alepherane 2-2 ndi Dedza Dynamos mmasewero omwe anaseweredwa pa bwalo la Kamuzu. Iye anati Bullets sinali bwino ndipo ikagonja mmasewerowa.
"Ndingowathokoza anyamata poti anabwera mmasewerowa ndikufananitsa mphamvu, masewero anativuta, Dedza inatipatsa ntchito yambiri ndipo timayenera kugonja koma anyamata anazipereka, kufanana mphamvu ndi kwabwino kwa ife." Iye anatero.
MacFarlane Mgwira ndi Hassan Kajoke anagoletsa zigoli ziwiri zomwe amabwenza pa zigoli za Clement Nyondo ndi Limbani Phiri kuti alepherane pa bwaloli. Bullets tsopano ili ndi mapointsi 26 pa masewero 13 mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores