MBC IWONETSA MASEWERO A MALAWI
Kanema wa dziko la Malawi, Malawi Broadcasting Corporation (MBC) walengeza kuti awonetsa masewero apakati pa Malawi ndi Lesotho omwe ndi ndime yamatimu anayi kumpikisano wa COSAFA mdziko la South Africa.
Mmodzi mwa akuluakulu a kanemayi, Chisomo Mwamadi, wati iwo apeza chilolezo choulutsa masewerowa pa MBC Tv, MBC 2 On the Go komanso Radio 2. Iye watinso ngati timuyi ifike ndime yotsiriza, iwo adzaonetsanso.
"Timu ya Flames yachita bwino kwambiri kumpikisanoeu, nde tinayesetsa ngati MBC kuti Mmalawi aliyense chimwemwechi chisamuphonye ndipo ndife okondwa kuti awonera pa MBC. Ngati Malawi ifike mu ndime yotsiriza ndekuti lamulungu adzawoneranso." Anatero Mwamadi.
Iye wati uwu ndi mwayi kuti makampani akatsatse malonda awo. Malawi ndi Lesotho onse anatsogolera gulu B ndi C aliyense kuti afike mu ndimeyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores