CHIWAULA WAPEREKA JERSEY KU CIVO
Mlembi wamkulu wakale kutimu ya Civo United, Ronald Chiwaula, wapereka ma jersey atsopano kutimu ya Civo lachinayi ku nyumba ya timuyi.
Chiwaula wati iye wachita izi kuti timuyi izimukumbukira poti kudziwa ntchito kwa iyeyu anayambira ku timuyi. Iye wati anawona chosowa chifukwa chake anabwerapo ndi kuthandiza.
"Ndisanapite ku SULOM ndinachokera kuno nde ndinaona kuti masewero 12 kapena 13 omwe asewera agwiritsa ntchito Jersey imodzi nde iyiyi iwathandiza kuti azisinthira. Ndikufuna adzindikumbukira ndi chifukwa chake pa mkono palembedwa dzina lomwe anandipatsa kutimuku loti Lonto." Iye anatero.
Chiwaula wati ndi wokonzeka kuthandiza timuyi ngati itamufikira koma zizitengera ngati iye azikwanitsa kutero. Iye anachoka kutimuyi pomwe anapeza mpando ku bungwe la Super League of Malawi chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores