KONDOWE WAKANA KUYANKHULA ATAGOLETSA CHIGOLI CHOYAMBA KU BULLETS
Katswiri wa timu FCB Nyasa Big Bullets, Ephraim Kondowe, wakana kuyankhulapo mmene akumvera pomwe wagoletsa chigoli chake choyamba kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe wati pakamwa patha kumusokoneza.
Kondowe anagoletsa chigoli chake choyamba chipitireni ku timuyi pomwe anamenya bomba atangosinthana ndi Antony Mfune pa mphindi 77 mmasewero omwe Bullets inagonjetsa Blue Eagles 3-0.
Mtolankhani wa Owinna, Hastings Kasonga, anafikira Kondowe kuti ayankhulepo pa chigolichi koma iye anati kuyankhulapo zikhoza kumupatsa phuma chifukwa akhonza kulonjeza zinthu zambiri komanso zovuta.
Iye wati adzayankhulapo kutsogoloku koma pakadali pano apitilizebe kukweza mutu kuti apangebe zambiri. Kondowe anapita kutimuyi kumayambiliro a chaka chino atachotsedwa kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers chaka Chatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores