"OSOKONEZA PA MASEWERO A BULLETS NDI WANDERERS ANJATIDWA" - MWAMADI
Mtsogoleri wa masapota a FCB Nyasa Big Bullets, Stone Mwamadi, walangiza masapota amatimu m'dziko muno kuti azivomereza matimu awo akagonja osati kuchita ziwawa.
Malingana ndi a Mwamadi , ati otsatira matimu m'dziko muno akuyenera kudziwa kuti mumpira mumakhala kugonja, Kupambana komanso kulepherana .
Iwo amayakhula izi kutsatira zomwe otsatira timu ya Mighty Mukuru Wanderers akhala akuchita kwa osewera awo masabata awiri apitawo kaamba koti timuyi sikuchita bwino.
Otsatira timu ya Mighty Mukuru Wanderers sabata yatha analetsa osewera a timuyi kukwera Bus yatimuyi atalepherana 1-1 nditimu ya Dedza Dynamos Salima Sugar FC pabwalo la kamuzu stadium.
A Mwamadi, achenjeza otsatira matimu a Mighty Mukuru Wanderers komanso Nyasa Big Bullets kuti yemwe angakapezeke akuchita zosokoneza masewero a Blantyre Derby omwe alipo loweruka lino adzanjatidwa, ndipo adzalandira chilango.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores