"NDI MOMWE TAKONZEKERERA MARAS ADZACHOKA AKUSANGALALA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United Abbas Makawa wamema otsatira timuyi kuti abwere mwamkokomo pabwalo la Civo chifukwa choti sadzachoka atakhumudwa pakutha pa masewero.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akukumana ndi Silver Strikers mu sabata yachisanu ndi chiwiri yamu FDH Premiership loweruka pakhomo pawo.
Iye wati akudziwa kuti akhala akuvutika ndi Silver chaka chatha koma ayesetsa mu masewerowa kuti akwanitse kuchita bwino.
"Takonzekera bwino kuti tidzachite bwino chifukwa takhala tikuvutika mu masewero angapo komanso anzathuwo akhala akuchita bwino kusonyeza kuti ndi masewero ovuta koma tidzayesesa," Iye anatero.
Makawa anatinso timu yawo yakwanitsa kukonza kutsogolo kwawo komwe kunali mavuto kamba koti amakwanitsa kupeza mipata koma amakanika kugoletsa.
Civil ikulowa mmasewerowa ili pa nambala 11 mu ligi pomwe ili ndi mapoints asanu ndi awiri (7) pa masewero asanu ndi imodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores