"Tayamba bwino mu Ligi" - Kananji
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake yayamba bwino mu Ligi ya chaka cha 2025 angakhale kuti angopambana kamodzi, kufanana mphamvu kamodzi ndi kugonjanso kamodzi mu Ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe timu yawo inalepherana 0-0 ndi timu ya Creck Sporting Club ndipo anati anali masewero ovuta kwambiri poti Creck imachokera kogonja mmasewero awiri.
Iye anati, "Tayamba bwino ngakhale kuti sitinapambane mmasewero onse Komabe Ifeyo tili ndi mapointsi anayi pomwe ena alibe Komabe tisakule mutu kuti tizitolabe mapointsi kupita chitsogolo." Iye anatero.
Timuyi tsopano yakwanitsa kutolera mapointsi anayi pa masewero atatu oyambilira mu Ligi ndipo ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7).
Pa 0991509953
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores