"MASEWERO AKADALI ONSE" - CHIMKWITA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Karonga United, Crispin Chimkwita, wati masewero awo ndi Mighty Wanderers ali ngati Chigawo chachiwiri chomwe ali ndi kuthekera kogoletsa zigoli ziwiri kuti afike mu ndime ya matimu anayi amu Airtel Top 8.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero achibwerenza amu chikho cha Airtel Top 8 omwe aliko pa bwalo la Karonga ndipo wati ndi zotheka kupambana mmasewerowo.
"Anatigonjetsa kwawo koma tsopano kuno ndi kunyumba tipange zotheka kuti tichite bwino. Masewero akadali onse ndipereke nzotheka kuti titha kugoletsa zigoli ziwiri ndi kupitiliranso." Iye anatero.
Timuyi ikupita mmasewerowo ikutsalira 1-0 poti inagonja mmasewero oyamba pa bwalo la Kamuzu ndi chigoli cha Blessings Mwalilino.
Opambana pa matimu awiriwa afike mu ndime ya matimu anayi ndipo adzakumana ndi opambana pakati pa Civil Service United ndi Mzuzu City Hammers.
paimeneyi 0995083970
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores