Mkulu oyang'anira aphunzitsi ku timu ya Ntopwa Isaac Jomo Osman wati ngakhale atuluka mu ligi ya TNM, koma Silver Strikers isayembekezere kutenga mapoint pamene akhale akusewera masewero masanawa.
A Osman ati Ntopwa yakonzeka kuchita bwino pa masewero ake awiri omwe atsala mu ligiyi.
Malingana ndi a Osman kutuluka kwawo mu ligi yaikulu mdziko muno ndi kaamba koti masewero anakhudzidwa kwambiri ndi matenda a Covid-19.
Silver Strikers isewera ndi timu ya Ntopwa masanawa pa bwalo la Nankhaka mu mzinda wa Lilongwe.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores