KHUDA WAPEREKA ULEMU KWA KAMBIRINYA
Katswiri womwetsa zigoli kutimu ya Masters FC Khuda Muyaba wapereka ulemu kwa katswiri wa Mighty Wanderers Alex Kambirinya kuti ali ndi tsogolo labwino.
Iye analemba uthengawu pa tsamba lake la mchezo kutsatira kuti anakumana kumathero a sabata yatha ndipo matimuwa analepherana 1-1.
Muyaba anatulutsidwa chigawo chachiwiri chikuyamba kuonetsa kuti analephera kuchita ntchito yoyenerera atatengedwa kwambiri ndi Kambirinya.
Iye analemba kuti, "Kambilinya 🙌 🇲🇼 replacement ya Mzava. No jealous koma ali mwala salute 🫡 nde chikupatsiratu osati kungochotsa eti bolla kuthazi ayi 🫵🏻 ambiri akugona."
Wanderers inagula Kambirinya kuchokera ku Mighty Tigers kutsatira kutuluka kwawo ndipo wakhala wosewera wodalilika ku Manoma chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores