Katswiri womwetsa zigoli kutimu ya Mighty Wanderers Blessings Mwalilino wasankhidwa kuti wasewera mwapamwamba kuposa aliyense mu mwezi wa June kutimuyi.
Mwalilino watenga mphotoyi atachita bwino pomwe anagoletsa ndi Creck Sporting Club mu Airtel Top 8 komanso kubwenza chigoli pomwe ankakumana Goshen City Dedza Dynamos.
Iye wapeza mavoti ochuluka pamwamba pa Felix Zulu komanso Promise Kamwendo ndipo alandira K400,000 komanso maphunziro oyendetsa galimoto a ndalama zokwana K1.1 million kuchokera ku Pemba Driving School.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores