"TIMU ILIPO NDIPO ZABWINO ZIKUBWERA" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers Lovemore Fazili wati timu yake yagonja ndi Ghana kamba koti amayesa osewera ena omwe samapatsidwa mpata ndipo ali ndi timu kale yomwe ibweretse zotsatira zokoma mu mpikisano wa Women's African Cup of Nations.
Iye anayankhula kutsatira kugonja 4-0 mu masewero otsiriza apaubale patsogolo pa mpikisanowu ndipo wati timu yake sinasewere bwino mu masewerowa.
Fazili anati osewera ena omwe anawapatsa mpata anasewera bwino ena zinawavuta komabe ali ndi chikhulupiliro kuti akhala ndi timu yabwino poyamba mpikisanowu.
"Zina zomwe taziona tizikonza komabe ndili ndi chikhulupiliro kuti ndili ndi timu yomwe tigwiritse mu mpikisanowu ndipo itibweretsera zokoma," anatero Fazili.
Iye watinso kusiya panja osewera ena odalilika ngati Tabitha Chawinga, Ireen Khumalo, Leticia Chinyamula komanso ena ndi kuwateteza kuti asavulale pomwe mpikisano watsala pang'ono.
Malawi iyamba masewero ake lachiwiri Sabata ya mawa pomwe idzaku
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores