MOLOGENI WASANKHIDWA KUKHALA KATSWIRI WAPAMWAMBA MU JUNE
Wotseka kumbuyo watimu ya FCB Nyasa Big Bullets Yamikani Mologeni wasankhidwa kuti ndi amene wasewera mwapamwamba kuposa aliyense mu FDH Premiership mu mwezi wa June.
Malingana ndi bungwe la Super League of Malawi, Mologeni anakwanitsa kuthandizira timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuchita bwino pomwe anasankhidwa kuti wasewera bwino pa masewero awiri omwe Bullets inakumana ndi Kamuzu Barracks komanso Masters FC.
Iye wagonjetsa katswiri wosewera pakati mutimu ya Civil Service United Righteous Banda komanso wotseka kumbuyo wa Silver Strikers Innocent Shema kuti atenge mphotoyi.
Mologeni, yemwe mphunzitsi wake Wedson Nyirenda anayamikira kuti ndi makina, alandira ndalama zokwana K300,000 kamba kopambana mphotoyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores