"KUBWERA KWA TEMWA KUTITHANDIZA KUPEZA ZIGOLI" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers Lovemore Fazili wati chidwi chake ayika kwambiri pa kupeza zigoli kutsogolo kww timuyi mu masewero opimana mphamvu omwe asewere ndi dziko la Ghana lachinayi mdziko la Morocco.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ndi otsiriza kumbali ya timuyi pokonzekera mpikisano wa Women's African Cup of Nations omwe uyambe pa 26 July 2026.
Iye wati kubwera kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa timuyi Temwa Chawinga kuwathandizira kukwanilitsa zimene akufuna kuti apeze zigoli zochuluka patsogolo pa mpikisanowu.
"Kuti tipeze chipambano ndi Ghana zitithandiza kwambiri chifukwa zitipatse molalo pomwe tikupita mu mpikisanowu ndiye paliponse tagwira tikungoyang'ana gawo la kupeza zigoli," anatero Fazili.
Aka ndi koyamba timuyi kuti isewere mu mpikisano wa WAFCON ndipo Fazili wati sakupitako kukasewera koma kukagwira ntchito ndipo sazisinthasint osewera ngati akuwayesa.
Matimu awiriwa anakumananso mu masewero ap
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores