MITHI NDI WOSEWERA WAPAMWAMBA MU MAY
Katswiri womwetsa zigoli kutimu ya Mighty Wanderers Lameck Mithi wasankhidwa kuti ndi yemwe anasewera mwapamwamba kuposa aliyense mu FDH Premiership mu mwezi wa May.
Mithi anakwanitsa kusewera masewero asanu ndi amodzi pomwe anayi anayamba ndipo awiri anachokera panja koma anamwetsa zigoli zisanu mu mweziwu.
Iye watenga mphotoyi atagonjetsa Webster Mzunda wa Blue Eagles komanso Ernest Petro wa Silver Strikers ndipo apatsidwa ndalama zokwana K300,000 kamba ka mphotoyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores