Otsatira timu ya Scorchers ali ndi chiyembekezo tsopano kuti timuyi ikhonza kuchita bwino ku mpikisano wa Women's African Cup of Nations kutsatira kugonja 2-1 ndi Morocco lachinayi.
Masewerowa anali pobisa kuti asaonetsedwe kuopa adani a timuyi kudziwa mphamvu zawo patsogolo pa mpikisanowu.
Malawi inatsalira 1-0 pa nthawi yopumulira kenako inagoletsako chigoli kuti agonje 2-1 kuzitolera pa kugonja 4-2 pa masewero omwe anakumana chaka chatha.
Malingana ndi ndemanga zaku tsamba la Football Association of Malawi zaonetsa kuti chiyembekezo chilipo kuti timuyi itha kuchita bwino kutengera kuti amakumana ndi timu 69 yapadziko lonse komanso inali kwawo pomwe Malawi ili pa 152.
Scorchers iyamba mpikisano wawo ndi kukumana ndi Nigeria pa 29 July 2026 isanakumanenso ndi Egypt komanso Zambia.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores