"TIKUFUNA TIZINDIKIRE CHOMWE TILILI KUNOKO" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers Lovemore Fazili wati masewero awo apaubale ndi Morocco awathandizira kwambiri kuti akwanitse kuona pomwe ali patsogolo pa mpikisano wa Women's African Cup of Nations.
Fazili amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko lachinayi ku Morocco komweko nthawi ya 9 koloko usiku ndipo aseweredwa kopanda ochemerera.
Iye wati akufuna atsikana adziwe kuti sanapite mdzikolo kukasewera koma kukagwira ntchito ndipo kupambana ndi Morocco kubweretsa molalo yapadera kwa osewerawa.
"Ndi masewero ofunikira chifukwa ationetsa cholinga chomwe tabwerera kunoko, osewera onse ali okonzeka bwino ndipo ndili ndi chiyembekezo kuti mavuto omwe takhala nawo mu masewero athu mmbuyomu akonza," anatero Fazili.
Iye anatinso alandilidwa bwino ndipo palibe chovuta chilichonse chifukwa nyengonso ndi yofanana ndi ya ku Malawi kuno poti kukutentha.
Malawi inakumana ndi Morocco pa masewero apaubale Chaka chatha ndipo ankatsogola 2-0
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores