FAM YAVOMEREZA BWALO LA NANKHAKA
Bungwe loyendetsa mpira mu dziko lino ya Football Association of Malawi pansi pa mbali ya First Instant Body yavomereza bwalo la Nankhaka kuyamba kuchititsa masewero amu ligi yaikulu m'dziko muno.
Izi zikudza bungweli litayenderanso bwaloli kutsatira kuti silinafikire mulingo ulendo womwe anayendera mu mwezi wa March koma pano eni bwaloli akonza zonse.
Kutsekedwa kwa bwaloli kunachititsa timu ya Blue Eagles kumakasewerera masewero ku bwalo la Civo ndipo kumathero asabatayi akuyenera kupita ku Mchinji pa bwalo la Aubrey Dimba ngati sipakhala kusintha.
Padakali pano, mabwalo a Kamuzu ndi Mzuzu omwe anakanika kufika mulingo woyenera pamodzi ndi bwalo la Nankhaka akadali otseka.
Bwalo la Kamuzu likugwiritsidwa ntchito ndi boma kulandira athu omwe akuchokera mdziko la South Africa pomwe bwalo la Mzuzu likadakonzedwabe.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores