MWANZA STARS YALEMBERA SRFA KUNENEZA BULLETS RESERVE
Timu yomwe ikusewera nawo mu ligi ya SRFA FINCA Division League One yalembera kalata bungwe loyendetsa ligiyi la Southern Region Football Association kuneneza timu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve kuti inagwiritsa ntchito osewera osalembetsedwa pa masewero omwe anakumana sabata yatha.
Mu kalata yomwe yalembedwa ndi kusainidwa ndi wapampando wa timuyi, Oscar Tobias Simfukwe, yati Bullets Reserve inachita zimenezi pa masewero awo otsegulira ligi pa bwalo la Joyce Chitsulo ku Mwanza ndipo anagonja 3-2.
Iwo ati bungweli lichitepo kanthu pa nkhaniyi kamba koti matimu onse anauzidwa kuti kupanga mchitidwewu ndiye kuti ndi kugawa mapoints aulere kutimu inayo.
Angakhale kuti kalatayo yalembedwa, timuyi sinatchulemo dzina la osewerawo omwe ikuwaganizira kuti sanalembetsedwe.
Padakali pano, sitinamve ngati kalatayo yafika ku bungwe la SRFA kuti odandaulawa athandizidwe.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores