FAM IKUYAMBITSA CHIKHO NDI LIGI YA MATIMU ANG'ONOANG'ONO
Bungwe la Football Association of Malawi likhazikitsa chikho cha matimu ang'onoang'ono a matimu omwe akusewera mu ligi yaikulu ya mdziko muno Chaka chino pofuna kukonzekeretsa matimuwa ku ligi yomwe idzayambe chaka cha mawa.
Izi zadziwika lachiwiri pomwe bungweli lalengeza kuti komiti yawo yaikulu inavomereza kuyamba kwa ligiyi Chaka cha mawa ndipo yayamba kale kukonzekera kuyamba kwa ligiyi.
Iwo ati akukhulupilira kuti ligiyi ipereka mpikisano wabwino kwa matimuwa komanso kukweza kasulidwe ka osewera, kukweza mpikisano komanso kukonza njira yopambana ya osewera omwe akuphukira kumene.
Malamulo a ligiyi ndi oti matimu ake azikhala okha omwe akusewera mu ligi yaikulu ya Chaka chimenecho ndipo kutuluka kwa timu yamu ligi yaikulu kuzitulutsanso yaing'ono yakeyo mu ligimu.
Chikho chomwe chiseweredwe chaka chino pa matimu aang'onowa sichikhala chotolera mapoints ngati ligi koma mwa kapha kachoka kuli kukonzekera kubwera kwa ligi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores