Bwalo la milandu loona za malamulo a ntchito lalamula bungwe la Football Association of Malawi kupereka ndalama zokwana K53.6 million kwa Patrick Mabedi kamba kochotsedwa ntchito mosatsata malamulo.
Woyimira mlandu wa Mabedi, Counsel David Kanyenda, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati tsatanetsatane wina wa chigamulochi afotokozabe.
Mabedi anachotsedwa ndi FAM kamba kusakhutira ndi zotsatira za pa ntchito yake ndipo anagwirako miyezi 11 yokha pa mgwirizano wa zaka ziwiri wake.
Pa dandaulo lake Ku bwalo la milandu, Mabedi anati akufuna K916 million kamba ka kachotsedwe ntchito kake.
Source -Times
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores