DEDZA YANYAMULITSIDWA NJERWA ZOOTCHA NDI AIGUPUTO KU ZOMBA
Timu ya Goshen City Dedza Dynamos yayamba movutika mu ligi ya chaka chino pomwe yagonjanso kachiwiri mu masewero atatu 3-0 ndi Red Lions pa masewero omwe anaseweredwa pa bwalo la Zomba lamulungu.
Timuyi yangokwanitsako kupeza point imodzi itafananitsa mphamvu mu masewero awo oyamba koma yakanika kumwetsako chigoli mu masewero aliwonse mosiyana ndi momwe ankachitira nthawi yokonzekera ligi.
Mphunzitsi watimuyi Alex Ngwira wati timu yake sinasewere bwino mu masewerowa zomwe zawapangitsa kuti agonje mopweteka motere.
"Ndi zokhumudwitsa kuti lero osewera akanika kutsatira zomwe timawauza komabe mpira ndi masewero 30 tibwerera tikakonze mavuto athu kuti masewero akubwerawo tidzachite bwino," anatero Ngwira.
Timuyi tsopano yatsika kufika pansi penipeni pa ligi pomwe ili ndi point yokwana imodzi pa masewero atatu omwe yasewera mu ligi ya FDH Premiership.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores