Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"TIKUFUNITSITSA CHIPAMBANO KUPOSA CHITIPAYO" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake ikufunitsitsa kuchita bwino mmasewero awo kusiyana ndi Chitipa United pomwe yati ikufuna kumatolera ma points masewero omwe akusewera.
Iye amayankhula patsogolo pokumana ndi Chitipa United lamulungu pa bwalo la Karonga ndipo wamema masapota awo kufika pa bwaloli kuti adzawapatse mphamvu.
"Ndi masewero ovuta kutengera kuti anzathuwa akuchoka kogonja komabe ifeyo tikufunitsitsa chipambano kuposa iwowo. Mbiri simagwira ntchito awa ndi masewero ena nde masapota abwere tiwapatsanso zosangalatsa." Anatero Kajawa.
Timuyi inayamba ndi kupambana 1-0 mmasewero awo oyamba mu ligi ndipo tsopano Ali pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) ndi mapointsi atatu.
Chitipa 0 FCB nyasa bb 0
hawadi juma
"TIKAYESETSA KUTI TICHITE BWINO" - MWASE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati timu yake yakonza mavuto omwe timakumana nawo mmene amasewera ndi Kamuzu Barracks ndipo akuyembekezeka kukachita bwino ku Mulanje.
Mwase amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi FOMO pa Mulanje Park Stadium ndipo wati akachita chilichonse chothekera kuti akapambane masewerowa.
"Takonzeka bwino kwambiri ndipo tinayamba ndi kulepherana ndi KB ndipo mavuto athu takonza, tikukumana ndi FOMO ku Mulanje omwe ndi masewero ovuta koma tikayetsetsa kuti tipambane." Anatero Mwase.
Iye wamema Manoma kuti afike pa bwaloli kuti akayipatse moto timuyi pomwe ikukalavula moto ku Mulanje.
Wanderers ili pa nambala Khumi (10) my ligi pomwe ili ndi point imodzi pa maseweronso amodzi.
"TAKONZEKA BWINO KUTI TIPAMBANE" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake yakonzekera kwambiri ndipo aliyense akufuna atatenga mapointsi atatu lamulungu.
Iye amayankhula patsogolo pokumana ndi timu ya Moyale Barracks lamulungu pa bwalo la Civo ndipo wati alibe phuma lililonse pa anyamatawa koma akungofuna kuti azichita bwino mmasewero awo.
"Takonzekera kwambiri masewerowa mukudziwa Moyale ndi timu ina yabwino koma anyamata akudziwa kufunikira kopambana masewerowa ndipo aliyense akufuna 3 points. Tilibe phuma lililonse, awa ndi ana nde sitingawapatse phuma lililonse tikungofuna tizichita bwino mmasewero omwe tikumenya basi." Anatero Nginde.
Timu ya Creck inayamba mwapamwamba mu ligi ya TNM pomwe inagonjetsa Waka Waka Tigers 3-1 ndipo padakali Pano ili pa nambala yachitatu mu ligi.
"BULLETS NOT AFFECTED BY MISSING PLAYERS" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, said his team was not affected by the absence of 13 players who are suffering from flu saying the team failed to show on the ground.
Pasuwa said this after their 0-0 draw against Mighty Waka Waka Tigers to collect just two points from possible 6 and said his team did not come to the party on Saturday.
"It was a tough game as we didn't do better in the middle of the park and slowly in build ups so that affected us not to get much spaces and create chances that could have been goals. I said we need to be a complete team and we are still learning." Said Pasuwa.
He further said he did not miss the players as ever player signed by Bullets should be ready to play when needed by the team.
Bullets are 9th on the table with two points taken from two games. They have scored just one goal and conceded one as well.
"BAKA CITY ILI NDI TSOGOLO LABWINO" - MUYOMBE
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Davie Muyombe, wati timu yake ikhale ikuchita bwino muligi ya TNM mmasewero akutsogoloku kamba koti akadaphunzira mmene mpira wamu ligiyi umayendera.
Iye amayankhula atagonja 2-1 ndi timu ya Mzuzu City Hammers kuti akhale masewero awiri opanda chipambano ndipo wati timu yake ndi yabwinobwino komanso ili ndi tsogolo labwino.
"Palibe mavuto aliwonse timu ilibwinobwino kungoti mwina poti tikumenya ligi yaikulu koma tiphunzira mmene mpira wake umayendera nde tikasewera masewero asanu kapena kudutsa apo tidzachita bwino kwambiri." Anatero Muyombe.
Iye anatinso masewerowa akanakhala ophweka kuti apambane koma ziganizo zina za oyimbira sizinali zabwino mmasewerowa.
Timuyi ili pa nambala 15 pomwe ilibe point iliyonse pa masewero awiri amene Iwo asewera.
"ANALI MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati timu yake inayilora Civo kuti ipatsirane kwambiri mchifukwa chake sinakwanitse kuyigwira mpaka agonja.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Civo ndipo wati kutsegula komwe anachita mchigawo chachiwiri kunangowaputira nkhondo pomwe anapezetsa chigoli chachiwiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tonse sitimachokera ku zotsatira zabwino koma tinawalora anzathu kukhala ndi mpira zomwe zinawapatsa mpata kuti apeze chigoli. Mchigawo chachiwiri tinasintha kuti tipanikize koma anagoletsa zomwe zinawafoola anyamata." Anatero Bunya.
Timuyi ikumane ndi Silver Strikers mmasewero awo otsatira ndipo ili ndi point imodzi pa nambala 13 pa masewero awiri mu ligi.
"TINAYICHENJERERA DEDZA KUTI TICHITE BWINO" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati chigoli cha msanga chinawathandiza kuti achite bwino ndipo ndi wokondwa kamba kopambana.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-0 ndi Dedza Dynamos ndi zigoli za Kelvin Kadzinje, Muhammad Biason komanso Emmanuel Savieli ndipo wati awalimbikitse osewera ake kuti azichitabe bwino.
"Anali masewero ovuta koma tinawachenjerera anzathuwa pomwe chigoli cha msanga chinatithandiza kwambiri kuwafoola koma tachita bwino, ku Mzuzu sabata yatha tinasewera bwino koma kuphonya nde lero tinawalimbikitsa, inde taphonya koma chipambano timachifuna Kwambiri." Anatero Makawa.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachiwiri mu ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi atatu pa masewero awiri omwe yasewera.
"TIMAFUNA IWO ASAMENYE IFENSO TISAMENYE" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Leo Mpulula, wati cholinga choika osewera ambiri pakati pomwe amakumana ndi Bullets chinali kuwatseka kuti timuyi isakhale ndi mpira komanso kugoletsa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati ndi okhutira kamba Ka mmene osewera anachitira mmasewerowa.
"Anali masewero ovuta kwambiri omwe tinaika osewera ambiri pakati kuti Iwo asamenye mpira chabwino ifenso tisamenye koma timangofuna kuwatseka kuti asagoletse. Tinapeza mipata taphonya koma ndiwayamikire anyamata asewera bwino." Anatero Mpulula.
Iye wati timuyi sinamalizike kugwirana ndipo ali osewera achisodzera omwe awagwiritsenso ntchito mu ligi ya chaka chino.
Tigers ili pa nambala 12 pomwe ili ndi point imodzi pa masewero awiri omwe iyo yasewera.
"OYIMBIRA WALERO SAMATHA KUIMBIRA" - KAMANGA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, walavulira khala la Moto kwa oyimbira, Lameck Manda, kuti samatha kugwira ntchito poti ziganizo zimamuvuta kupanga.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi MAFCO pa Chitowe ndipo ziganizo za oyimbira sizinali zabwino Kwa iwo.
"Oyimbira masewero awawa sanatikonde ndipo uyuyu samatha kuimbira, tinabweraponso pano anawononga masewero nde tisamayesane ngati olephera chifukwa timagwira ntchito kukonzekera basi nkumabwera kudzaononga zinthu, sindikuti MAFCO yachinya chigoli cholakwika koma samadziwa ziganizo." Anatero Kamanga.
Kamuzu Barracks ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi awiri pa masewero awirinso omwe yasewera.
"NDAKHUTIRA NDI ZOTSATIRAZI" - GONDWE
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Stereo Gondwe, wati wakhutira ndi zotsatira zomwe timu yake yapeza pomwe yafanana mphamvu 1-1 ndi timu ya Kamuzu Barracks pa bwalo la Chitowe loweruka.
Gondwe anati timu yake inayesesa mpaka kupeza chigoli nthawi yothaitha ndipo akukhulupilira kuti akhale akuchita bwino mu masewero apatsogolo pawo.
"Anali masewero ovuta tithokoze Mulungu kuti tapeza point imodzi. Anzathuwa anachinya patali kwambiri ndipo zimaoneka ngati zitivuta koma sitinatope, tinayesetsa mpaka tinapeza chigoli kutatsala mphindi zitatu." Anatero Gondwe.
Timu ya MAFCO tsopano ili pa nambala 11 ndi point imodzi yomwe ayipeza atasewera masewero awiri mu ligi.
MZUZU CITY HAMMERS ILI PAMWAMBA PA LIGI
Timu ya Mzuzu City Hammers ikupitilira kuchita bwino pomwe yapambana masewero awo achiwiri mu ligi pogonjetsa Baka City 2-1 pa bwalo la Mzuzu.
Isaac Msiska komanso Yasin Rashid anamwetsa zigoli zatimuyi pomwe Joseph Mwambungu anapeza chopukutira misonzi zomwe zinakondweretsa mphunzitsi wamkulu, Elias Chirambo.
"Ndine wokondwa kwambiri kamba koti tapambana, sabata yatha tinavutika popita kutsogolo nde tinakonza mavuto athu, tasewera bwino ndipo tapambana. Sine wokhutira ndi mipata yomwe taphonya poti tinakonza kwambiri kutsogolo nde tikakonzanso." Anatero Chirambo.
Hammers tsopano ili pamwamba pa ligi ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6) omwe awapeza pa masewero awiri omwe yasewera.
BULLETS STRIKE ANOTHER DEAL
FCB Nyasa Big Bullets has entered into an agreement with Paramount Concrete Company that will be awarding player of match with a miniature and K75,000.
This has been disclosed during a press conference held by the team on Friday where the signing of the contracts between the two companies was done.
Chief Executive Officer at Paramount Concrete Products, Arthur Kalinde, Said Bullets gives them a platform to get their products known to people as it is a big brand. He said he will be hoping to come back again when the contract ends after this season.
Meanwhile, Chief Administration Officer at Bullets, Albert Chigoga, said their award winning brand is an attraction to other companies to partner the team and the team will work with every company partnering with them.
The first recipient of the award will be known on Saturday as FCB Nyasa Big Bullets play Mighty Waka Waka Tigers at the Kamuzu Stadium.
📷: George Sulumba
"WAMKULU AKACHOKA AKULIRA PA MULANJE" - FOMO
Mkulu woona za malonda ku FOMO, Daniel Mbebuwa, wati timuyi ili ndi mapointsi asanu ndi imodzi kale angakhale kuti sanasewere ndi Mighty Mukuru Wanderers ponena kuti Manoma akachoka manja ali mkhosi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa omwe achitike pa bwalo la Mulanje lamulungu ndipo wachenjeza a Wanderers kuti akonzekere mikango yolusa yokhayokha.
"Ndiwauze kuti sabata yatha tinamasula mikango yaimuna yokha koma apa tikamasula yaimuna ndi yaikazi ndipo akonzeke kudzathamanga, wamkulu adzachoka akulira chifukwa Pano ndi pamanda." Anatero Mbebuwa.
Iye wamema anthu kuti akhamukire ku bwaloli poti kudzakhalanso kugulitsa kwa unifolomu ya timuyi patsikuli.
Timuyi ikuchokera kopambana 1-0 ndi Bangwe All Stars ndipo inakumana ndi Manoma chaka chatha mu Castel Challenge ndipo Wanderers inapambana 1-0.
Noma 2:1fomo prediction
HAMMERS YAWINA K90 MILLION KU BETIKA
Kampani yopanga za mlosera ya Betika yasainirana mgwirizano wa zaka zitatu ndi timu ya Mzuzu City Hammers omwe timuyi izilandira K30 million pa chaka chilichonse.
Mgwirizanowu wasainidwa lachisanu ku Mzuzu komwe mwa zina amaulula zamumgwirizano wawo komanso kuonetsa unifolomu yomwe agwiritse ntchito chaka chino.
Wapampando watimuyi, Gift Mkandawire wati ndi wokondwa kamba Ka thandizoli pomwe lithandize kuti timuyi iyende bwino mu zaka zitatu zikudzazi.
"Matimu ang'onoang'ono ngati ifeyo timakumana ndi mavuto osiyanasiyana nde anzathuwa abwera nthawi yabwino atithandizako kuchepetsa mavuto omwe timakumana nawo." Anatero Mkandawire.
Ndipo mkulu wa kampani ya Betika, Gift Govati, wati akufunitsitsa atatukula luso la mchigawo chakumpoto poti kwa nthawi yaitali limavutika kuti lionedwe ndi anthu.
Timuyi iyamba kugwiritsa ntchito makaka olembedwa Betika loweruka pomwe akukumana ndi Baka City pa bwalo la Mzuzu mu masewero awo achiwiri amu 2024 TNM Su
"TAKONZEKA MMENE TIMACHITIRA NTHAWI ZONSE" - GONDWE
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Stereo Gondwe, wati timu yake yakonzeka mmene imachitira pa masewero aliwonse ndipo alibe phuma lopambana masewero.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi Kamuzu Barracks loweruka ndipo wati iwo asewera mmene amachitira nthawi zonse.
"Takonzekera mmene timapangira nthawi zonse anyamata alibwino ndipo mawa agwira ntchito. Chipambano amapereka ndi Mulungu nde masewero angoyamba kumene tilibe phuma lililonse." Anatero Gondwe.
Timuyi inayamba ligi ya chaka chino moipa pomwe inagonja 2-1 ndi asilikali anzawo a Moyale Barracks sabata yatha.
"IT'S A MUST WIN AGAINST HAMMERS" - MUYOMBE
Baka City interim coach, Davie Muyombe, said he is targeting a win as they play Mzuzu City Hammers on Saturday at the Mzuzu Stadium so that it brings the confidence of players in the season.
Muyombe said this on Friday ahead of the match and said the departure of Oscar Kaunda has seen some things sorted at the club and is looking to perform well this season.
"We are well prepared for the match, our training had been good and the boys are in good shape, no injuries and we are out to win. A win will help to bring molare to the team so that we start winning games so we are ready." Said Muyombe.
He further confirmed that the players that missed their league opener last weekend have been cleared and will play against Hammers.
The rookies suffered a 0-1 defeat against Karonga United in a Kyungu derby last week and they are the only rookie not to have a win this season.
CIVO YAKONZEKA KUKUMANA NDI DEDZA
Timu ya Civo United yati yakonzeka kukumana ndi Dedza Dynamos loweruka likudzali ndipo ikufunitsitsa itapeza chipambano kuti mitima ikhazikike kutimuyi.
Mphunzitsi watimuyi, Abbas Makawa, wati timu yake yamaliza zokonzekera zawo ndipo wati osewera Ake akudziwa kufunikira kopambana pakhomo ndikuti ayiwale kugonja Kwa sabata yatha ndi Mzuzu City Hammers.
"Tamaliza bwino zokonzekera ndipo zayenda bwino kwatsala ndi pabwalo, takonzekera kuti tikachite bwino chifukwa tinagonja mophweka sabata yatha pomwe tinamenya bwino koma sitinapeze chigoli nde mawa tigwira ntchito." Anatero Makawa.
Timu ya Civo inayamba moipa pomwe inagonja 1-0 ndi Mzuzu City Hammers yomwe inangokwanitsa kumenyera pagolo kamodzi kokha basi.
CHAWINGA BAGS ANOTHER AWARD IN FRANCE
Scorchers forward, Tabitha Chawinga, has won her second award of the season after named as the Soccer Hearts Player of the month of March.
This follows an impressive performance in the month of which she has managed to score a goal or more in every game she has played in the month.
This is her second award after winning the D1 Arkema player of the month of March last month.
NO HISTORY IN FOOTBALL FOR PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, has downplayed the fact they have dominated Mighty Waka Waka Tigers for the past 13 years saying history has no effect in Football.
The Zimbabwean tactician was speaking to the team's media on Friday ahead of Saturday's match against the Kau Kau boys at the Kamuzu Stadium and he said Tigers is one of the teams that gives them headache when playing them.
"I think in Football we don't talk history but the amunition that you are having in that particular year, if you prepare yourself to do go you will do good, I think it's one of the things we have to look at ourselves if we are prepared to face Tigers. This is one of the teams that gives us a tollid time because they prepare on everything in the game," highlighted Pasuwa.
The Kau Kau boys have lastly beaten the People's team on 20 August 2011 where they won 0-3 at the Kamuzu Stadium and in 13 years, their best result has been a draw.
"ITS A TRICKY GAME AGAINST BANGWE" - MPONDA
Silver Strikers head coach, Peter Mponda, said facing Bangwe All Stars will be one of the tough games to play as they are facing a good team.
Mponda said this on Friday ahead of their Sunday's meeting with Bangwe All Stars at the Silver Stadium and said his team is ready to keep momentum of winning games in the current season.
"It's a tricky one. We faced them during Pre-Season and they are a good team, good on the ball and their defense is hard to unlock but I think we are well prepared and with the speed that we have when attacking will help us to get through their defense but it's s tricky one." Said Mponda.
He said it is important for their team to win on Sunday as they don't want to drop any point when playing home and also show seriousness of competing for Championship this season.
Last season, the Bankers beat Bangwe 4-1 in the first round but had to be stunned at the Kamuzu Stadium in a 3-2 defeat in the second round.
📷: Silver
"ZIGOLI ZAVUMBA KWAMBIRI PA ZOKONZEKERA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Christopher Nyambose, wati timu yake sipita mophweka ku Lilongwe kukakumana ndi Silver Strikers kamba koti mitima ikuwawa ndi kugonja kwa FOMO sabata yatha.
Mphunzitsiyu amayankhula lachisanu pomwe amamalizitsa zokonzekera za masewerowa omwe aliko loweruka pa bwalo la Silver ndipo wati kubwera kwa Clever Chikwata kwapangitsa zokonzekera zawo kukhalanso zabwino.
"Zokonzekera zayenda bwino kwambiri anyamata onse alibwino ndipo akuchilimika ndasiyanitsa ndi za sabata yatha poti panopa zigoli zikuvumba ndipo anyamata ndi owawidwa ndi kugonja ndi FOMO nde masewero awa tikupita kukapambana zikavuta kufanana mphamvu." Anatero Nyambose.
Iye anati Silver Strikers ndi timu yabwino yomwe ili ndi aphunzitsi komanso osewera odziwa ndipo akuipatsa ulemu koma kumbali yawo akonzeka.
Atakumana chaka chatha, Silver inapambana 4-1 ku Lilongwe ndipo Bangwe inapambana 3-2 ku Blantyre.
PHODO OUT FOR FIVE WEEKS
FCB Nyasa Big Bullets forward, Maxwell Gasten Phodo, will not be available for five weeks after sustaining an injury during the team's 1-1 draw against Dedza Dynamos in their league opener last weekend.
Phodo was heavily tackled on the 25th minute of the game and was stretched off with the goal scorer of the match, Ephraim Kondowe replacing him in the match.
Following his injury, the team's Coach, Callisto Pasuwa was left fuming as he blamed the referees for not protecting his players.
"One thing I will talk about officiation. What they are doing is not fair and each and every game I keep on complaining I think they have to be professional for the goodness of our game, look today, I have lost another player and even no card was given but if it was us a card could have come out," spoke Pasuwa.
Meanwhile, the former Silver Strikers forward has been reported to miss five games due to the injury.
The People's team play Mighty Waka Waka Tigers on Saturday in
TWO MALAWIANS SIGN DEALS IN ICELAND
Two Youngsters from Malawi, Precious Kapunda aged 19 and Levison Munyenyembe aged 18, have signed deals for Icelandic club, UMF Afturelding from Ascent Academy after having successful trials at the team.
The two stars went to the team in January and have won the hearts of the team thereby signing for this upcoming season.
Kapunda and Munyenyembe have become the first Ascent Academy players to sign pro-contracts in Europe.
Source: Ascent Academy Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
predictors
"OYIMBIRA AYAMBA BWINO KWABASI" - KALICHERO
Mlembi wa bungwe la oyimbira mdziko muno, Chris Kalichero, wayamikira oyimbira a mdziko muno kuti ayamba bwino pomwe agwira ntchito yapamwamba mu sabata yoyamba ya ligi.
Kalichero wayankhula izi ngakhale kuti aphunzitsi ena adandaulapo ndi mmene oyimbira anachitira koma iye wati sangalephere anthu ena ongodandaula zabodza.
"Tithokoze oyimbira onse kuti achita bwino kwambiri ndipo ayamba bwino mwina asunga zomwe tinawauza kuti zomwe aphunzira azigwiritse ntchito. Pa anthu onse opita ku masewero sipangalepheredi odandaula koma onse tawaonera, palibe walakwitsapo." Anatero Kalichero.
Mu chaka chatha, matimu ochuluka anadandaula ndi kayimbilidwe ndiponso zipolowe zimayamba kamba mchitidwewu. Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Stereo Gondwe komanso Callisto Pasuwa wa Bullets anadandaulako za oyimbirawa mu sabata yoyamba yomweyi.
Firee manoma
Fire nyelere timayenda ngati msomba
Arsenal 3:1 buyen munich
Cheee
Arsenal 1-0 Bayern Munich
Games