Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"TIKUYENERA KUKONZA ZAMBIRI" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Leo Mpulula, wati timu yake ikufunika kukonzedwa mu zinthu zambiri angakhale kuti apambana pomwe wati siwokhutira ndi mmene amasewerera osewera ake.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mzuzu City Hammers 1-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati chipambanochi chakhala bwino pokonza mmene aonekere pa ndandanda wa matimu koma ali ndi ntchito yaikulu yokonza timuyi.
"Tithokoze osewera kuti tapambana koma tataya mipata yochuluka kwambiri zomwe zikutanthauza kuti tili ndi ntchito yaikulu yoti tikonze pa osewerawa komabe timafunika kuti tipambane kuti zisaipe pa tebulo koma ntchitoyo ndi yambiri yoti tikonze." Anatero Mpulula.
Tigers tsopano ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe yatolera mapointsi anayi (4) pa masewero atatu omwe yasewera.
"TIMAFUNA IWO ASAMENYE IFENSO TISAMENYE" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Leo Mpulula, wati cholinga choika osewera ambiri pakati pomwe amakumana ndi Bullets chinali kuwatseka kuti timuyi isakhale ndi mpira komanso kugoletsa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati ndi okhutira kamba Ka mmene osewera anachitira mmasewerowa.
"Anali masewero ovuta kwambiri omwe tinaika osewera ambiri pakati kuti Iwo asamenye mpira chabwino ifenso tisamenye koma timangofuna kuwatseka kuti asagoletse. Tinapeza mipata taphonya koma ndiwayamikire anyamata asewera bwino." Anatero Mpulula.
Iye wati timuyi sinamalizike kugwirana ndipo ali osewera achisodzera omwe awagwiritsenso ntchito mu ligi ya chaka chino.
Tigers ili pa nambala 12 pomwe ili ndi point imodzi pa masewero awiri omwe iyo yasewera.
Cheee
"LEROLI TINACHEPERA KABA" - ABAMBO
Mkulu watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Robin Alufandika, wavomereza kuti timu yawo sinali bwino ndipo akakonza monse molakwika akabwerera ku Blantyre.
Iye amayankhula kutsatira kugonja 3-1 ndi Creck Sporting Club pa bwalo la Civo masana a lamulungu ndipo wati timu yawo sinachite bwino mmasewerowa.
"Tivomereze zativuta mmasewerowa sitinakwanitse kuchita mphamvu zathu kuti tipambane, tachepera kaba ndipo anzathuwa atichinya." Anatero Abambo.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachikhumi ndi chisanu (15) poti ilibe point iliyonse ndiponso yagoletsetsa zigoli zitatu ndikuchinyako chimodzi.
CHIPUNGU IS TIGERS CAPTAIN
Mighty Waka Waka Tigers has announced the appointment of Precious Chipungu as the team's captain.
The Striker has been chosen due to the unavailability of the captain following the move of Masiya Manda to Civil Service United during the transfer window.
Meanwhile, Chipungu will be deputised by Kelvin Banda and Ben Manyozo in that order.
Tigers play Creck Sporting Club away at the Civo Stadium in their league's opener on Sunday.
LEO MPULULA AKUYAMBA NTCHITO MWEZI UNO
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers watsopano, Leo Mpulula, akuyembekezeka kuyamba ntchito kutimuku sabata ikudzayi pomwe timuyi ikuyamba zokonzekera mmwezi omwe uno.
Izi zikudza malingana ndi kulengeza kwa timuyi kuti ayamba zokonzekera za ligi ya chaka cha 2024 lolemba Pa 29 January pa bwalo la Mpira ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre.
Nthawi timuyi ikhala ikuyesanso osewera ena atsopano omwe ngati angachite bwino akasewerenso mutimuyi mu 2024.
Mpulula walowa mmalo mwa Christopher Nyambose yemwe anachotsedwa ndi timuyi kamba kosachita bwino pomwe anathera pa nambala 11 mu 2023.
GONDWE WACHOTSEDWA KU TIGERS
Katswiri wotseka kumbuyo ku Mighty Wakawaka Tigers, Sandress Gondwe, wachotsedwa ku timuyi pomwe mphunzitsi watsopano, Leo Mpulula, wamuuza kuti sali mu dongosolo lake.
Katswiriyu wauza Owinna kuti akuluakulu atimuyi anamufikira ndipo amuchotsa dzina lake mu kaundula watimuyi kusonyeza kuti ali ndi mwayi wosewera timu iliyonse.
"Ndi zoona, anandipeza akuluakulu ndipo andichotsa kuti ndikhonza kupita kulikonse. Ndi zowawa chifukwa sindinayembekezere komabe ndachilandira panopa ndadekha kaye kuti ndiwone komwe nditalowere." Anatero Gondwe.
Katswiriyu ali ndi tsoka pa Mpulula pomwenso mphunzitsiyu sanakondwere ndi ntchito zakenso ali ku Silver Strikers Reserve. Iye wati atiuza komwe alowere.
LEO IS BACK!!!
Mighty Wakawaka Tigers has announced Leo Mpulula as their new coach in the 2024 season replacing Christopher Nyambose.
Mpulula has penned a two year contract with the Kaukau Boys on Thursday.
MPULULA ALENGEZEDWA KU TIGERS
Timu ya Mighty Wakawaka Tigers yatsala pang'ono kumalizitsa zotenga mphunzitsi yemwe wachoka ku Silver Strikers, Leo Mpulula, kuti atsogolere timuyi mu chaka cha 2024.
Izi ndi malingana ndi zomwe tapeza kuti ligi ya chaka chatha itangotha, akuluakulu a timuyi anamupeza mphunzitsiyu kuti atsogolere timuyi ndi chifukwa chake anatsanzika ku Silver.
Mpulula akuyembekezeka kulengezedwa tsiku lililonse mu sabata yomwe ino kukhala mlowammalo wa Christopher Nyambose kutimuyi.
"TIGERS NDI TIMU YAIKULU SINGATULUKE" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati ananeneratu kuti Tigers ndi dzina lalikulu ndikuti singatuluke mu ligi ndipo zatsimikizika mtsiku lamulungu pa bwalo la Dedza.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi timu ya Kamuzu Barracks ndipo wati anali masewero ovuta kwambiri pomwe KB inabwera mwamphamvu kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri poti timasewera ndi timu yabwino komanso inadabwitsa kuti inabwera mwamphamvu kwambiri ngati mwina imamenyera abale awo kuti asatuluke nde komabe timayenera kuzimenyera nkhondo mpaka zatheka." Anatero Nyambose.
Iye anati timu yake inakumana ndi mavuto kamba koti anasintha osewera 7 atabwera kumene ndipo wathokoza SULOM kamba koyendetsa bwino ligiyi. Tigers yamaliza pa nambala 11 ndi mapointsi okwana 36 mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"INALI PLAN YATHU KUIKHUMUDWITSA WANDERERS" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati amadziwa kuti masewero awo ndi Mighty Mukuru Wanderers akhala ovuta kwambiri potengera kuti matimu onse amafunitsitsa mapointsi atatu.
Iye amayankhula atatha masewero omwe matimuwa alepherana 0-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati anyamata ake anachita zomwe anawauza kuti angowakhumudwitsa a Wanderers.
"Anali masewero othamanga kwambiri komanso ovuta kwambiri poti matimu onse amafunitsitsa chipambano. Ife tikuthawa kuti tisatuluke mu ligi komanso Wanderers imafuna kuti mwina ikokere chikho ku Lali Lubani komabe anyamata asewera bwino mpaka tatengako point imodzi." Anatero Nyambose.
Timu ya Tigers ili pa nambala 10 mu ligiyi ndi mapointsi 35 pa masewero 29 omwe yasewera ndipo yatsala kuti ikumane ndi timu ya Kamuzu Barracks koyenda kuti amalize ligi ya chaka chino.
"TINAWAUZA ANYAMATA KUTI AKAFERE MU BWALO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati ndi wokondwa ndi mmene timu yake inasewera ndi Moyale Barracks pomwe wati masewerowa amaonetsa tsogolo la timuyi mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anagonjetsa Moyale Barracks 3-0 pa bwalo la Kamuzu koma wati akufunikirabe kupambana mmasewero omwe atsala nawo kuti athere pabwino.
"Anali masewero ofunikira kwambiri potengera kuti amationetsa tsogolo lokhala mu ligi nde ndithokoze anyamata analimbikira kuchinya Moyale 3-0 si zophweka koma zatengera kulimbikira kwawo. Apapa ntchito ikadalipo chifukwa ligiyi yavuta kwambiri." Anatero Nyambose.
Iye anatinso kutsogola masewero omwe asewera kulibe ntchito koma kumapambana poti Fodya umanena wapamphuno. Tigers ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi 31 pa masewero 26.
#Tawonga2023
"UDZU WAKE NDI WAKUNYUMBA OSAYENERA PA BWALO LA MPIRA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati timu yake inavutika kuti isewere bwino pa bwalo la Rumphi kamba koti kapinga yemwe ali pa bwaloli amatelera kwambiri.
Nyambose amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 1-1 ndi timu ya Ekwendeni Hammers ndipo wati point yomwe atengayi iwathandiza kusokerera penapake pofunikira.
"Anali masewero abwino anyamata anayesetsa kuti asewere bwino koma kapinga ali pa bwaloli ndi uja amafunika kukhala kunyumba uja nde amatelera mwina pakufunikira kapinga uja ogwira uja kuti pasamatere. Ligi yavuta ndipo point iliyonse ikumakhala yofunikira kwambiri, point yalero itisuntha penapake." Anatero Nyambose.
Timu ya Tigers ili tsopano ndi mapointsi 28 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligiyi ndipo ili pa nambala yachikhumi.
PAJA WAMKULU AKAVUTIKA AMAMUTHANDIZIRA"" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati timu ya FCB Nyasa Big Bullets yachita kuthandizidwa ndi oyimbira kuti apambane mmasewero omwe matimuwa anakumana pomwe wati penate yomwe Bullets inapeza ndi yopatsidwa.
Nyambose amayankhula izi atatha masewerowa pa bwalo la Kamuzu pomwe Bullets yapambana ndi chigoli cha pa mphindi 88 za masewerowa kudzera pa penate. Iye wati timu yake yaphonya kwambiri komabe oyimbira wayithandiza Bullets.
"Ndi Zoona mchigawo choyamba tinasewera bwino kwambiri ndipo timapanga chilichonse koma mipata yathu sitinaigwiritse ntchito zomwe zinawathandiza anzathuwa kuti abweremo ndipo chigawo chachiwiri anali bwino komabe paja wamkulu ndi wamkulu akavutika amathandizidwa nde amuthandizadi." Anatero Nyambose.
Timu ya Tigers tsopano ikadali pa nambala 11 mu ligi pomwe yatolera mapointsi 27 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
"MPHECHEPECHE MWA NJOBVU SAPITAMO KAWIRI" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati sakufunanso kuti timu yake ibwererenso kumunsi kwa ligi komwe iwo anali kamba koti mmene ligi yavutiramu palibe timu yomwe ili pa mtendere.
Nyambose amayankhula izi timu yake itafika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) kutsatira kugonjetsa Red Lions 1-0 pa bwalo la Kamuzu. Iye anati timu yake sinasewere bwino koma zilibe ntchito pomwe pakadali pano chipambano nde chofunikira.
"Tiyesetsabe kuti tipitilize kupeza zipambanozi chifukwa mphechepeche mwa njobvu sapitamo kawiri, kumunsi kuja sitikufuna tibwererenso nde tiyesetsa kupambana mmasewero athu." anatero Nyambose.
Tigers yatsala ndi masewero asanu ndi atatu (8) kuti imalize ligi ya chaka chino ndipo yakwanitsa kutolera mapointsi 27 ndipo ali ndi mapointsi anayi pamwamba pa malo amatimu otuluka mu ligi.
"ODWALA TOKHATOKHA TAKUMANA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati masewero awo ndi timu ya Extreme FC masana a lachiwiri akhale ovuta poti matimu onse akufunitsitsa kutsala mu ligi koma ali kunsi kwa ligi.
Nyambose wayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati ngakhale kuti zinthu zikuvuta, timu yake ikupita mmasewerowa ndi cholinga chopambana mmasewerowa kuti achoke kumunsi kwa ligi koma watibe wakufa saopa kuola.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tonse takhalitsa ku mzere ofiira nde tikamakumana chonchi zimavuta komabe ifeyo takhalitsa kumene kuja, tikufunitsitsa titachokako kumene kuja kuti tifikire ku mtundako nde anyamata tawauza kufunikira kopambana masewero amenewa." Anatero Nyambose.
Iye wati masewerowa awatenge ngati a ndime yotsiriza poti sipabweranso ena kudzakumana ndi Extreme. Tigers ikuchokera kogonja 3-1 ndi Blue Eagles ndipo ili pa nambala 13 ndi mapointsi 18.
"NDI NTCHITO YAKE" - NYAMBOSE WAKANA KUKWEZA NYASULU MU MTENGO
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, anakanika kuyamikira goloboyi wa timu yake, Innocent Nyasulu, atachotsa mapenate awiri mmasewero omwe anagonjetsa Dedza Dynamos 2-0 ponena kuti ndi ntchito yake.
Nyambose anati chipambano cha timuyi chinabwera kudzera mu kulimbikira kwa ntchito zake ndipo Nyasulu monga wapagolo amayenera kugwiranso ntchito yake.
"Yah ndi mnyamata wabwino ndipo amatithandiza kwambiri, kuchotsa mapenate awiri ndi chinthu cha mtengo wapatali koma ngati amakhala pamene paja ndekuti ndi ntchito yake, ndife odala poti tili naye." Anatero Nyambose.
Nyasulu tsopano wachotsa mapenate asanu mu chaka chokha chino mu ligi ya TNM ndipo anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba mmasewerowa kachisanunso mu ligi ya chaka chino.
Tigers tsopano yafika pa nambala 11 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligiyi.
SAKA WAPITA KU TIGERS
Timu ya Karonga United yalengeza kuti katswiri wawo, Steve Saka, akupita kutimu ya Mighty Wakawaka Tigers pangongole kwa miyezi isanu.
Timuyi yalengeza nkhaniyi lachisanu ndipo iye tsopano akhonza kupezeka mmasewero omwe Tigers ikumane ndi Bangwe All Stars lachitatu likudzali.
Katswiriyu anachokera kutimu ya Dwangwa United kuti azipita ku Karonga.
"TIMAKONZA TSOPANO TIKOLOLE" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati timu yake tsopano ili bwino ndipo tsopano iyambe kukolola zomwe amafesa mchigawo choyamba.
Nyambose amayankhula izi atatha masewero omwe timu yake inalepherana 1-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Kamuzu lachitatu. Iye anali osangalala ndi kaseweredwe katimuyi ndipo wati mchigawo chachiwiri, iwo agwira ntchito yaikulu.
"Timu yathu sinatuluke koma kungoti kubwera kwa osewera atsopano ku timuyi kunapangitsa kuti zina zizivuta koma tsopano takonza ndipo taona kusintha lero tagoletsa chigoli chabwinobwino pomwe ndi Blue Eagles timaphonya kwambiri apa tiyamba kukolola zomwe timalima." Anatero Nyambose.
Iye anatinso ndi okondwa poti timu yake sikuchinyitsa kwambiri pomwe wati ndi Chitipa yokha yomwe inagoletsa zigoli ziwiri pa iwo. Timuyi yamaliza pa nambala 14 ndi mapointsi 14 mu chigawo choyamba.
"TIKUIKHUMBA BULLETS MPAKE TAITSATIRA KU KAMUZU STADIUM" - ABAMBO
Mkulu watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Robin 'Abambo' Alufandika, wati timu yake ikuyikhumba timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti akaikhomere pakwawo pomwepo pomwe matimuwa akukumana lachitatu.
Abambo ati akuyembekezera kuti masewerowa kukhala ovuta kwambiri ponena kuti matimu onsewa ndi apamwamba kwambiri ndipo masewero akhalenso apamwamba.
"Mbambande mbambande, paja mukudziwa kale kuti ifeyo ndi timu mbambande ndipo Bullets ndi mbambandenso ndipo masewerowa akakhalanso mbambande. Ifeyo tachita kuwatsatira pa bwalo lawo chifukwa tikuwakhumba ndipo mubwere mawa mudzaone nokha." Watero Alufandika.
Matimuwa akumane mmasewero awo otsiriza a mu gawo loyamba ya ligi ya TNM Supa ligi ndipo chipambano cha Bullets chiwatengere pa mapointsi 32 pomwe Tigers idzafika pa mapointsi 16 ngati idzapambane.