Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"TADANDAULA KWAMBIRI NDI OYIMBIRA" - CHAFERAMTHENGO
Mphunzitsi watimu ya Durban FC yaku Balaka, Chikondi Chaferamthengo, wati ndi wodandaula kwambiri kamba koti iwo ndi timu yaing'ono ndi yakumudzi kwambiri yomwe yangotolera luso la osewera koma oyimbira sanayimbire mowakonda.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-2 ndi timu ya Bangwe All Stars ndipo wati aphunzirapo zambiri pa masewerowa koma oyimbira sanawakonde.
Masewerowa oyimbira anaonjezera mphindi zokwana khumi pomwe masewero anali pa 2-2 ndipo mkatikati mwa mphindizi Bangwe All Stars inapeza chigoli kudzera mwa Beston Jimu.
Iye anati, "Anali masewero abwinobwino tasewera bwino mmene tinakonzera. Ifeyo ndi timu ya ana yakumudzi yomwe tangoyitolera ndipo tikuyimanga kumene komano zikamachitika ngati zomwe achita oyimbira nde kupha luso la osewera nde tingopempha kuti ngati tikufuna mpira wathu ukome oyimbira agwire ntchito yabwino."
It anatinso mmidzi muli osewera ambiri aluso omwe ali ndi kuthekera kopita patsogolo
koma adindo sakuyikapo chidwi potukula lusoli.
Zateremu timuyi yatuluka mu chikho cha Castel Challenge mu ndime ya matimu 32 ndipo Bangwe All Stars yapitilira ndipo idzasewera ndi timu ya FOMO.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr