"OSEWERA A BULLETS ASIYA POMPANO" - MISELENI
Mphunzitsi wa timu ya osewera akale a Mighty Wanderers, Darlington Miseleni, wati timu yake inachepera mphamvu poti osewera ake ambiri anasiya mpira kalekale kuposera a Bullets omwe asiya mpira posachedwa.
Iye amayankhula kutsatira kugonja kwawo 3-1 ndi timu ya Bullets mu Premier Bet International Legends Cup pa bwalo la Kamuzu masana a loweruka.
Iye wati zawapweteka poti akanika kuteteza chikhochi komabe iwo sakuyang'ana pansi.
"Ifeyo mphamvu tinachepekedwa kusiyana ndi anzathu a Bullets omwe mpira asiya pompano koma athu anasiya kalekale mafuta mu thanki anatha." Anatero.
Wanderers ikumana ndi Dynamos yaku Zimbabwe polimbirana pa nambala yachitatu lamulungu pa bwalo lomweli.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores