"NDALAMA ZAKE ZIKUTHANDIZA KWAMBIRI" - JOSSAM
Yemwe amaphunzitsa timu ya osewera akale a FCB Nyasa Big Bullets, Mzee Jossam, wati ndalama zomwe timuyi ikumapeza potenga nawo mbali pa masewero osiyanasiyana zikuthandizira osewera ena akale.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mighty Wanderers 3-1 kuti afike ndime yotsiriza yamu Premier Bet International Legends Cup loweruka pa bwalo la Kamuzu.
Iye anati Wanderers anayiwerenga bwino ndipo kusintha kwawo mchigawo chachiwiri kunathandiza kuti achite bwino ndipo ayimenya Wanderers opandanso mvula.
Iye wati wakondwa kuti akumana ndi Silver Strikers yomwe imawathawa kwambiri komabe wamema ochemerera kubwera ku masewerowa.
"Tiwapemphe kuti abwere mwaunyinji, mipikisanoyi ikutithandiza kwambiri chifukwa pompano tinakathandiza Lloyd Nkhwazi apa tipita kwa Alex Masanjala, zambiri zikubweranso." Anatero Jossam.
Zigoli za Robert Ng'ambi ziwiri ndi chimodzi cha John Lanjesi ndi zomwe zathandiza timuyi kuchita bwino pomwe Victor Nyirenda anagoletsera Wanderers.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores