Haiya: Akadzakanika kupita ku AFCON 2027 adzachoka
Mphunzitsi watsopano kutimu ya Flames, Kalisto Pasuwa, wapatsidwa milingo yoti adzatengere Malawi ku mpikisano wa African Cup of Nations mu 2027, adzatengeko COSAFA mu zaka ziwirizi komanso pa masewero opitira ku World Cup omwe atsala asanu ndi imodzi adzapambaneko atatu.
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, ndi yemwe anatsimikiza za nkhaniyi pa mwambo omuonetsa mphunzitsiyu.
Iye wati mulingo wopita ku AFCON 2027 nde omwe akufunikira kuti akwanilitse afune asafune ndipo ngati sadzatero adzachoka.
"Iyo ya AFCON nde yomwe ayesetse komanso pa zaka zakezi tikufuna COSAFA, mwina chaka choyamba chomanga timu ndipo chinacho atha kudzatero. Komanso masewero aku World Cup tipambaneko atatu." Anatero.
Iye koma wati ngakhale zili momwemo, bungweli lithandize kwambiri Pasuwa kuti akwanitse kuchita bwino pa ntchito yake.
Pasuwa atsogolere timuyi posachedwapa mu mpikisano wa CHAN wa masewero opitira ku mpikisano wa World Cup omwe anayamba kale kusewerako.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores