Pasuwa, Mponda alimbirana mphoto
Kalisto Pasuwa, yemwe anali wa FCB Nyasa Big Bullets ndi Peter Mponda, yemwe anali ku Silver Strikers, alinbirane pa mphoto ya mphunzitsi wabwino mu chaka cha 2024 pa mwambo womwe bungwe la Football Association of Malawi likhale likupereka mphoto.
Mwambo wopereka mphotozi uliko pa 21 February 2025 ndipo FAM yasankha Pasuwa, Mponda komanso Eliya Kananji wa Blue Eagles kuti alimbirane pa mphotoyi.
Pasuwa, yemwe tsopano wachoka ku Bullets, anawina chikho cha Airtel Top 8 ndi timuyi pomwe Mponda, yemwe pano ali ku Bullets, anatenga supa ligi ndipo Kananji anatenga FDH Bank komanso kuyibwenzeretsa timu yake mu ligi yaikulu.
Ku mbali ya mphoto ya aphunzitsi a mpira wa amayi, Maggie Chombo wa FCB Nyasa Big Bullets Women, Thom Nkolongo wa Ascent Academy ndi Linda Kasenda wa Civil Women ndi omwe akupikisana.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores