ABAMBO: TIGERS IKUFUNA OWATHANDIZA
Mkulu watimu ya Mighty Tigers, Robin Abambo Alufandika, wamema makampani ndi anthu akufuna kwabwino kuti abwere adzathandize timu mbambande poti padakali pano alibe owathandiza.
Alufandika amayankhula atafunsidwa momwe chaka cha 2025 akonzera kuti agwire ntchito ndipo wati makampani sadzakhumudwa poti Tigers simatuluka mu ligi.
"Timu mbambande ilibe wowathandiza chaka chino nde timeme makampani ndi akufuna kwabwino kuti abwere, iyi ndi timu mbambande, ankhala kale mu ligi, akatswiri odziwa kusula osewera ndipo sadzakhumudwa." Anatero Abambo.
Iye anatinso mu chaka cha 2025 si chaka choyankhula Kwambiri koma chogwira ntchito ndipo akufuna kuti apange zokupsa.
Matiga omwe anatengako ligi mu chaka cha 1989 anamaliza pa nambala 12 chaka chatha ndipo ayamba zokonzekera pa 21 January 2025 pa bwalo la Mpira.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores