Wosewera wa FCB Nyasa Big Bullets, Hassan Kajoke tsopano ndimfulu poti wabweza ndalama yokwana MK3.9 million.
Bungwe la FAM linalamula katswiriyu kuti abweze ndalamazi atalepherana ndi Silver Strikers pankhani za mgwirizano.
FAM linamupatsa Kajoke masiku asanu kuti ngati satero, sadzaseweranso mpira mdziko muno ndi kunja.
Tsamba la Wa Ganyu latsimikiza kuti Kajoke wabweza ndalamayi komanso MK 200, 000 ngati chindapusa ku bungwe la FAM.
Pano wosewerayi ndi mfulu kusewera mpira tsopano.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores