Katswiri wa FCB Nyasa Big Bullets,Hassan Kajoke sanapelekebe ndalama zomwe anauzidwa kuti kuti atero ndi bungwe la FAM pasanathe masiku asanu.
Kajoke anauzidwa kuti abweze ndalama zokwana K3.9million zomwe anasayina ngati mgwirizano ndi Silver Strikers chifukwa ndondomeko zambiri zinaphwanyidwa.
Kulephera kupeleka masikuwa atadusa Kajoke azalesedwa kusewera mpira mdziko muno komanso kunja, FAM inatero.
Pofika lero Silver Strikers kudzera mwa mlembi wa board a Peter Masiye ati timuyi yatumiza ndalama zokwana K900, 000 zomwe anauzidwa ngati chindapusa.
Choncho Silver Strikers yapempha FAM kuti liletse Kajoke kuti asiye kusewera mpira chifukwa sanakwanilise zomwe anauzidwa kuchita.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores