Usiku wathawu akuluakulu a Malawi Council for Sports ndi a Football Association of Malawi anali mkachipinda komwe amakambirana za tsogolo la mphunzitsi wamkulu wa timu ya dziko lino, Mario Marinica.
Mwa zina amaunikira momwe Marinica wachitira ndi Flames ndipo amvana zoti mgwilizano wake ukafika kumapeto pa 30 April mwezi wa mawa sakuyenera kupatsidwanso mgwilizano wa tsopano.
Choncho lero Football Association of Malawi ikumana ndi mphunzitsiyu kuti amudziwitse izi kuti akhoza kudikilabe kufika pa 30 April kapena atuliletu pansi udindo chifukwa sapasidwanso kontrakiti ina.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores