Bungwe lomwe limayang'anira mpira la FAM lanena kuti iwunikila bwino m'mene mphunzitsi wa Malawi wachitira kontrakiti yake ikatha pa 5 April.
A Marinica adasankhidwa kukhala mphunzitsi wa Malawi chaka chatha ndipo adasayina kotrakiti ya chaka chimodzi.
Izi zikudza pamene pali maganizo a anthu osiyanasiyana kuti mwina mphunzitsiyi apasidwe kontrakiti ina kapena ayi kutsatira kusachita bwino kwa Flames mu ndime yozigulira malo mu AFCON.
A Marinica poyankhila pankhani yakusachita bwino kwa Flames ati satula pansi udindo kufikira kontrakiti yawo itatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores