"CHILIMBIKITSO CHATHU NDI SCORCHERS" - CHIKHOSI
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers Ladies Andrew Chikhosi wati ali ndi timu ya osewera yomwe ikhoza kukafika patali ndipo chilimbikitso chawo ndi timu ya Scorchers.
Iye amayankhula pomwe timuyi yaikidwa mu gulu B ya mpikisano wa CAF COSAFA Women's Champions league Qualifiers pa mayere omwe bungwe la COSAFA linachititsa lachiwiri kummawa.
Silver yaikidwa pamodzi ndi matimu a Mamelodi Sundowns yaku South Africa, Nsingizini Hotspurs yaku Eswatini komanso Costa do Sol yaku Mozambique mu gululi lomwe ndi lovuta kwambiri.
Chikhosi wati anali akudziwa kuti mayere ake akhala ovuta kwambiri ndipo sakuchita kamba koti sanapiteko ku mpikisanowu.
"Nayo Scorchers anthu amayinena koma yapanga zozizwitsa chomwe chili chilimbikitso chathu. Mu timu ija muli osewera asanu athu zomwe zikuoneka kuti tikadzawaphatikiza ndi ena ali kuno tidzapanga zozizwitsa," anatero Chikhosi.
Silver inakwanitsa kuzigulira malo ku mpikisanowu itatenga ukatswiri wa ligi yaikulu ya mdziko muno yachaka chatha.
Aka kakhala koyamba kuti Silver Strikers Ladies ipite ku mpikisanowu pomwe Kukoma Ntopwa Queens yapitako kawiri pomwe Ascent Soccer Academy yasewerako kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores