KHUDA WACHOKA KU MASTERS
Katswiri wosewera kutsogolo mu timu ya Masters FC Khuda Muyaba wachoka kutimuyi kutsatira kumvana kwa mbali ziwirizi kuti zitero.
Malingana ndi mmodzi mwa olemba nkhani mdziko muno Twaha Chimuka, Muyaba samagwirizana ndi mphunzitsi Peter Mponda koma timuyi yati ili mbali ya mphunzitsi wawo ndipo yemwe sakugwirizana naye achoke ndi iyeyo.
Ndipo Katswiriyu akhale akubwenza ndalama zomwe anatenga atasaina mgwirizano wake kutimuyi kutsatira zomwe onse agwirizana.
Muyaba anapita ku Masters masabata atatu apitawa ndipo wangoseweratu masewero awiri okha ndi kuthandizira zigoli ziwiri komanso kutenga mphoto ya osewera wapamwamba pa masewero kamodzi.
Source : Twaha Chimuka.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores