Joseph: Mulungu amudalitse Mponda pondikumbukira
Wosewera watsopano ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Blessings Joseph, wati wathokoza kwambiri kwa mphunzitsi Peter Mponda pomwe wamukumbukiranso ndi kumukhulupilira kuti atha kugwiranso ntchito limodzi.
Iye amayankhula atasaina mgwirizano wa zaka zitatu kutimuyi pomwe tsopano wachoka ku timu ya Chitipa United ndipo wati ndi wokondwa popita ku Bullets.
Iye wati zikuonetsa kuti Mponda amakhala akumutsatabe kulikonse amayenda ndipo asewera chimodzimodzi momwe amachitira ku Chitipa.
"Chitipanso ndi timu yaikulu ndipo ngati ndimasewera bwino Bullets ndi kundiona ndekuti ndi zotheka kuseweranso kunoko nde ndilimbikira kuchepetsa kulakwitsa kuti anthu atikonde." Anatero Josephy.
Katswiriyu wasewerapo timu ya Wizards yomwe inali ya Mponda mu zaka khumi zapitazo ndipo uku ndi kukumananso kwa iye ndi mphunzitsiyu.