Pogba ndi mfulu tsapano
Katswiri yemwe kwawo ndiku France ndipo wasewerako matimu a Juventus komanso Manchester United, Paul Pogba, akuyembekezeka kuyambanso kusewera mpira pomwe wathana nacho chilango chake.
Pogba wasowa mwa kanthawi tsopano pomwe analandira chilango kuti asasewere mpira kwa zaka zinayi (4) kamba kopezeka olakwa pogwiritsa ntchito mankhwala oonjezera mphamvu mthupi.
Koma mkatikati mwa chilangochi, chinachepetsedwa kufika pa miyezi khumi isanu ndi itatu (18 months) ndipo chatha dzulo laliwisili.
Katswiriyu yemwe anapambanako World Cup mu chaka cha 2018, akadalibe timu koma mphekesera zikumveka kuti atha kusewereranso Manchester United, Fulham, Inter Miami kapenanso matimu a mdziko la France lomweli.
#UCL #football #team #Owinna#UEFA
Come on fulham fada
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores