SAVIELI WATSANZIKA KU EKHAYA
Katswiri womwetsa zigoli kutimu ya Ekhaya, Emmanuel Savieli, watsanzika kutimuyi kutsatira kutha kwa mgwirizano wapangongole.
Savieli analemba uthenga pa tsamba lake la mchezo la Facebook kuthokoza osewera anzake, aphunzitsi ndi akuluakulu atimuyi pomusamalira nthawi yomwe anali ndi timuyi.
Savieli anali pa ngongole kuchokera kutimu ya Mufulira Wanderers yomwe inamugula kuchokera ku FCB Nyasa Big Bullets ndipo amafuna apeze nthawi yosewera yochuluka ku Ekhayako.
Iye wakwanitsa kumwetsa zigoli zisanu ndi timuyi mu ligi ya TNM ndipo nthawi yochuluka ya ligiyi wakhala ali wovulala.
📷: Ekhaya media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores