NYONDO WATHOTHOLEDWA KU TIMU
Timu ya Highlanders yalengeza kuti yachotsa osewera okwana asanu ndi atatu kuphatikizapo osewera wa mdziko muno, Atusaye Nyondo.
Timuyi yachita izi pofuna kukonzanso kuti akhale ndi timu yapamwamba mu chaka cha 2026.
Iye anapita kutimuyi ndi mphunzitsi wake wakale ku Silver Strikers, Peter De Jongh yemwe wachokanso kutimuyi, kuchokera ku timu ya Casric Stars yaku South Africa.
Nyondo wakhalw osewera wachiwiri waku Malawi kuchotsedwa ku Zimbabwe pomwe Vincent Nyangulu anathotholedwa ndi FC Platinum.
Omwe achotsedwa ndi awa: - Melikhaya Ncube - Mckinnon Mushore - Mthabisi Ncube - Honest Mhlanga - Nqobile Ndlovu - Martin Nhubu - Atusaye Nyondo - Learnmore Muyambo
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores