SULOM yatsegula milandu kwa Silver, Ekhaya ndi Elias Missi
Bungwe la Super League of Malawi latulutsa milandu yomwe matimu a Silver Strikers, Ekhaya FC komanso wotseka pagolo wa Ekhaya, Elias Missi akuyenera kuyankha pochita zinthu zina zosaloledwa ku mpira.
Bungweli lapeza milandu yokwana itatu Silver Strikers yomwe ndi kukanika kuletsa masapota awo kupanga zolakwika ngati kuthira zamadzi kwa osewera a MAFCO komanso kuwaopseza, kusokoneza chitetezo cha osewera ndi oyimbira ndi kuipsa mbiri ya ligiyi.
Ndipo bungweli lapezanso Ekhaya yolakwa kamba kolowetsa masewero a mpira wamiyendo ku chisokonezo ndiponso goloboyi wawo ayankha pa mlandu yopanga zinthu zosakhala za mpira pokhwinya Babatunde Adepoju pakhosi.
Silver inapalamula milanduyi pomwe imakumana ndi MAFCO pa bwalo la Silver omwe analepherana 0-0 pomwe Ekhaya ndi Missi anachita izi pomwe anagonja 0-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets ma sabata atatu apitawo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores