Masewero amu ligi ya TNM ayimitsidwa kale mu sabata khumi ya mpikisanowu poti timu ya dziko lino ikupita ku mpikisano wa chikho cha COSAFA ku South Africa.
Bungwe la Super League of Malawi ndi lomwe lalengeza za izi ndipo lati Masewero adzayambiranso mpikisanowu ukatha.
Mpikisanowu ukuyamba pa 04 June 2025 ndipo udzatha pa 14 June 2025 ndipo osewera omwe apita kumeneko ochuluka ndi omwe amasewera mu matimu a mdziko lino.
Masewero otsiriza a sabata yachisanu ndi chimodzi aseweredwe mtsiku la lero pamene Mighty Tigers ilandire timu ya Moyale Barracks pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.
Masewero ayima pomwe matimu ena asewera kale Masewero asanu ndi atatu pamene ena asewera asanu okha kapena asanu ndi amodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores