"Anyamata anayesetsa tiwayamikire" - Mhone
Mphunzitsi watimu ya Songwe Border United, Enock Mhone, wati ngakhale kuti timu yake yagonja 7-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets, osewera ake anayesetsa mu zinthu zingapo mmasewerowo.
Iye amayankhula atatha masewerowa pa bwalo la Kamuzu ndipo anavomereza kugonja kwawo ponena kuti amakumana ndi timu yaikulu komanso kuti osewera ambiri ndi achisodzera oti sanasewerepo ligiyi.
Iye anati: "Tiwayamikire osewerawa mbali zina achita bwino sangayipe konse ndikukhulupilira kuti masewero atsala ambiri ndipo mpata ulipo oti titha kudzachita bwino."
Uku tsopano ndi kugonja kwachitatu kwa timuyi mmasewerowo atatunso pomwe tsopano ali pa nambala 16 opanda point ndipo sanachinyeko koma achinyitsako 12.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores