SULOM yapempha makampani kuthandiza matimu onse
Bungwe loyendetsa ligi yaikulu ya mdziko muno la Super League of Malawi yapempha makampani osiyanasiyana kuti athandize matimu onse mu ligiyi kuti mpira wa mdziko muno upite patsogolo.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungweli, Ronald Chiwaula, amayankhula izi usiku wa lachitatu pa mwambo womwe timu ya Civil Service United imapereka mphoto kwa osewera awo omwe anachita bwino mu chaka cha 2024.
Iwo anayamikira Kampani ya Tree Business Suppliers kamba kothandiza timuyi ndi K50 million ndipo wati zikanakoma makampani ambiri atathandizanso matimu 16 onse amu ligi.
"Itati K50 million imeneyi ikumapita kumatimu onse 16 amuligiyi ndekuti Zitha kukhala bwino ndikupepukanso chifukwa mpira wathu timavutika chifukwanso chosowa ndalama mmatimumu." Iye anatero.
Iye wapemphanso boma kutsitsa msonkho wa kampaniyi kuti phindu lawo lizipita ku timuyi kapena kuwapatsa ntchito zinanso kuti zawo ziziyenda.
Matimu ena ngati Mighty Tigers, Chitipa United, Son
Songwe Border United komanso Karonga United ndi ena mwa matimu omwe asewere chaka chino opanda thandizo lolozeka.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores