LUANAR YAPATSIDWA MILANDU ISANU NDI UMODZI
Bungwe loyendetsa mpira mchigawo chapakati lapereka milandu isanu ndi Imodzi kutimu ya LUANAR kutsatira zipolowe zomwe anachita pa masewero omwe anagonja 1-0 ndi TN Stars pa bwalo la Mbavi lachitatu lapitali.
Mu kalata imene yasainidwa ndi mlembi wamkulu wa bungweli, Antonio Manda, lapeza timuyi ndi milandu isanu ndi umodzi kuti iyankhe.
Milanduyi ndi kulephera kuteteza osewera awo ndi masapota kuchita ziwawa, kumenya oyimbira, kubilibinya nthumbi ya bungweli, kulowetsa chiwawa mu masewero a mpira wamiyendo komanso kunyazitsa mbiri ya bungweli komanso omwe amathandiza ligiyi a Chipiku Stores.
Timuyi yapatsidwa maola 24 kuti iyankhepo ndi yankho lolemba pa milanduyi ndipo kulephera kutero bungweli lipitilira ndi zilango zomwe lakonza.
Mmasewerowa, osewera anayamba kumenya oyimbira kusakhutira ndi mmene anagwilira ntchito yake ndipo ochemerera nawo anachitanso chimodzimodzi.
Masewerowa anali achipulula ofuna kupeza timu yomwe isewere nawo
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores