Kampani ya GM Plastics yalonjeza kupereka K100, 000 kwa osewera anayi omwe asankhidwe kuti asewera bwino pa masewero a mu mpikisano wa Betika Sapitwa Big Four omwe wuchitike kumapeto a sabatayi.
Kampaniyi yalengeza za izi patsogolo pa mpikisanowu omee ukhale ukuyamba loweruka pa 22 March mpaka pa 23 March 2025.
Iwo atinso osewera yemwe adzasankhidwe kuti wasewera bwino mu mpikisanowu adzalandira ndalama yokwana K150, 000 Kuchokera ku Kampaniyi.
Matimu a Mighty Tigers ndi Ekhaya ndi omwe akuyamba kusewera mu mpikisanowu nthawi ya 12 koloko asanabwere matimu a Creck Sporting Club ndi FCB Nyasa Big Bullets nthawi ya 3 koloko masana.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores